Yesu anachita chozizwitsa chodyetsa anthu 5,000 ndi mikate isanu yabalere m’chipululu kutsidya lina la nyanja ya Tiberiya. Koma Iye adati kwa iwo, “Musagwire ntchito chifukwa cha chakudya chimene chimaonongeka, koma chakudya chimene chipirira kufikira ku moyo wosatha.” Kotero, Iye anawalola iwo kudziwa za mkate weniweni wopatsa moyo.
Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa nachiritsa anthu ambiri, koma onse anafa. Kuchiritsidwa ku matenda kapena kukhalanso ndi moyo si chozizwitsa. Kupeza moyo wosatha pakusunga Paskha, umene uli mwambo wa kudya mkate wa moyo; ndi chozizwa chachikulu.
“Tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” Monga Petro, ana a Mulungu ayenera kupereka mayamiko ndi ulemerero kwa Mulungu powapatsa mphatso ya moyo wosatha.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi