Amai Akumwamba Yerusalemu, Gwero la madzi amoyo.
Mulungu Amaperekabe Mzimu Woyera Kumalo Kumene Kumachitika Phwando la Misasa
Anthu amene amakhulupirira Mulungu ayenera kusunga Phwando la Misasa motsatira ziphunzitso za Mulungu. Izi zili choncho chifukwa Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Zekariya kuti adzapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amasunga Phwando la Misasa ndi kubweretsa chilango kwa iwo amene salisunga.
Mpingo wa Mulungu Umasunga Phwando la Misasa, ndipo Uli ndi Mzimu ndi Mkwatibwi, Amene Amapereka Madzi Amoyo
Pa kubwera Kwake koyamba, Yesu anapereka Mzimu Woyera; pa kubwera Kwake kwachiwiri, Mzimu ndi Mkwatibwi amapereka Mzimu Woyera pa Phwando la Misasa. Maulosi a m’Baibulo akuti, “Mzimu ndi Mkwatibwi amapereka madzi amoyo,” “Madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu,” ndi “Mtsinje wa madzi amoyo umatuluka pa mpando wa chifumu wa Mulungu” akuneneratu kuti Amai Akumwamba a ku Yerusalemu adzapereka Mzimu Woyera ndi ziphunzitso zotsogolera ku moyo.
Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.
Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena,...
Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.
Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire...
Yohane 7:2–39
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.
Chivumbulutso 22:17
Nambala ya Owonera84
#Madyelero a Misasa