Ziyeneretso zolowera mu ufumu wa kumwamba ndi za anthu okhawo amene amachita chifuniro cha Mulungu. Baibulo ndi uthenga wa Mulungu wa chipulumutso kwa anthu onse, wolembedwa ndi aneneri omwe anatsogoleredwa ndi Mzimu Woyera kuti alembe chifuniro Chake. N'chifukwa chake Mulungu analamula kuti tisawonjezere kapena kuchotsapo mawu ake.
M’Baibulo, Mulungu amatchulidwa m’njira yochuluka, osati m’modzi, pafupifupi nthawi 2,500. Komanso, Baibulo limatsimikizira kuti monga momwe mayi alili m'dziko la zomera ndi dziko la zinyama zomwe zinalengedwa motsatira chifuniro cha Mulungu, momwemonso mu ufumu wakumwamba, pali Mulungu Amai, amene amapereka moyo wosatha, ndipo palinso banja lathu lauzimu lakumwamba.
Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu, ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse. 2 Akorinto 6:17–18
Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu. Agalatiya 4:26
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi