Gideoni anali wamng’ono m’banja lake ndipo anali wa fuko lofooka kwambiri mwa mafuko onse a Isiraeli. Komabe anatha kugonjetsa amuna a ku Midyani okwana 135,000 ndi asilikali 300 okha mwa kumvera mawu a Mulungu. Mose ndi Yoswa anagonjetsanso Aamaleki pomvera mawu a Mulungu. Mofananamo, ngakhale lero, kupambana muzochitika zonse kumabwera chifukwa cha kukhulupirira thandizo la Mulungu ndi kumvera Iye.
Monga momwe Yesaya analoserera, “Mulungu adzayesa waung’ono mtundu wamphamvu,” awo amene amazindikira kuti chirichonse padziko lapansi chikuchitika mogwirizana ndi dongosolo la Mulungu ndi kumvera mawu a Mulungu, ngakhale m’chinthu chooneka ngati chaching’ono, adzadalitsidwa.
Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka mu Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga. Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi
Oweruza 6:15-16
Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe. Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake.
Yesaya 60:21-22
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi