Pamene tilibe chikhulupiriro, nyengo zotizungulira zimapitabe m’njira yolakwika.
Tikakhala ndi chikhulupiriro, zonse zimayenda bwino.
Tiyenera kuzindikira mfundo imeneyi kudzera m’Baibulo ndi kutaya mantha, nkhawa ndi zovuta zathu zonse m’moyo wathu wachikhulupiriro.
Baibulo limakamba za ntchito ya Gideoni, ntchito ya Yoswa, ntchito yogawa Nyanja Yofiira, ndi mikate isanu yabalere ndi nsomba ziŵiri.
Zinkaoneka ngati zosatheka m’maso mwa anthu, koma Mulungu anachita zonse.
Momwemonso, ngati tikhulupirira mawu a Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi ndi ziphunzitso za Yesu zakuti uthenga wabwino wa pangano latsopano udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zonse zidzakwaniritsidwa molingana ndi mawu Awo.
Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo.
Aroma 14:23
Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.
Marko 9:23
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi