Mu nthawi ino, Khristu Ahnsahnghong anabwera padziko lapansi monga momwe kunaloseledwera, anakhazikitsa Mpingo wa Mulungu, ndipo anadziwitsa Amai Akumwamba Yerusalemu, ndikunena kuti, “Ndimatsatira Amai.” Monga momwe kunaloseledwera, ulemerero wa Amai Akumwamba Yerusalemu wakhala kuwala kwa chiyembekezo m'dziko lamdima lino.
Pamene mamembala anawalitsa kuunika kwa Yerusalemu, akukhulupirira kuti uwu ndi uthenga wabwino wotsogozedwa ndi Mulungu, anthu a zilankhulo ndi zikhalidwe zosiyanasiyana ochokera padziko lonse lapansi akufulumira kubwerera ku Ziyoni. Kwa ana Ake amene anakhulupirira maulosi ndi kuwalitsa ulemerero wa Amai Akumwamba Yerusalemu, Mulungu amakwaniritsa lonjezo Lake: “Adzakhala nawo kwamuyaya—inde, kwamuyaya muyaya.”
Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako. Yesaya 60:2–3
Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya. Daniele 7:18
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi