Mtumwi Paulo anakhala mneneri wamkulu chifukwa adaona ulemerero wa kumwamba kwachitatu. M’chilengedwe chonse chachikulu chimene anthu sangathe kuchimvetsa, Mulungu watikonzera tsogolo laulemerero. Ichi ndichifukwa chake watiitana kuti tikhale ndi kawonedwe kokulirapo, kuti tisayang’ane dziko lapansi, koma chilengedwe chonse—ndiko, ku ufumu wa kumwamba.
Tiyenera kugonjetsa mavuto a lero poyang’ana pa ulemerero wa ufumu wa kumwamba ndi tsogolo lowala limene likutiyembekezera kumeneko. Ngati tilephera kukhulupirira ufumu wa kumwamba, pamapeto ake tidzataya chikhulupiriro chathu pakati pa kuvutika kwakanthawi ndikusiya choonadi. Komabe, ngati timvetsetsa zenizeni za ufumu wa kumwamba, chikhulupiriro chathu chidzakula tsiku ndi tsiku, kutithandiza kutenga nawo mbali mu ulemerero wake.
pakuti chisamaliro cha thupi ndi imfa; koma chisamaliro cha mzimu ndi moyo ndi mtendere. Aroma 8:6
Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro. Aroma 8:24–25
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi