Tikaganizira za moyo wathu, timazindikira kuti talandira thandizo kuchokera kwa mlangizi nthawi zambiri kuti tifike kumene tili lero.
Simungathe kuchita zonse mwangwiro nokha popanda kulandira thandizo kuchokera kwa wina.
M'mawu ena, gawo lalikulu la kupambana kwathu limadalira yemwe ali mlangizi wathu.
Masiku ano, Mpingo wa Mulungu wa Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse ukupitirizabe kukula ndi kudabwitsa dziko lapansi.
Mpingo wa Mulungu walandira mphotho zosiyanasiyana za pulezidenti, monga U.K. Queens Mphoto za Ntchito Zongozipereka, ma Satifiketi atatu osiyanasiyana a pulezidenti ku Korea, ndi Mphoto za Ntchito Zongozipereka ku US.
Ndindani yemwe ali mlangizi wa Mpingo wa Mulungu umene unapangitsa kuti ukhale wopambana kwambiri?
“Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13)
Mneneri Yesaya analosera kuti Mulungu adzakhala mlangizi wathu.
Mu Yesaya "ana ako" akutanthauza ndani?
Tikamawerenga mavesi apamwambapa, timazindikira kuti "ana ako", akuimira ana a mzinda wa Yerusalemu.
Ndiye, kodi Yerusalemu akuimira yani?
Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu. (Agalatiya 4:26)
Zoona za Yerusalemu ndi Amayi athu a Kumwamba.
Choncho, ana awo ndi amene adzakhaladi oyenera kulowa ufumu wakumwamba.
Mpingo wa Mulungu ndi mpingo wokhawo masiku ano umene umakhulupirira Mulungu Amayi.
Amayi athu akumwamba, omwe aali nafe lero, ndi mlangizi wa Mpingo wa Mulungu.
Pachifukwa chimenechi, Mpingo wa Mulungu umapambana m'zonse zimene umachita.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi