Bukuli limanena kuti gawo lodabwitsa kwambiri ndi Genesis, pamene Mulungu akutchedwa kuti “ife.” Pamene Mulungu Atate analenga munthu, sananene kuti,
“Ndipange munthu . . . ,” koma Iye anati, “Tipange munthu . . ”Genesis 1:26
Mulungu ndi mmodzi, “Atate”! Nangano n’chifukwa chiyani Mulungu amatchulidwa kuti “ife” m’Baibulo?
“Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”Genesis 1:1
Mu Torah, malemba oyambirira a Baibulo, analembedwa kuti “Elohim” kutanthauza “Milungu.”
Elohim amatanthauza “Milungu” monga kuchulukitsa kwa “El” kapena “Eloah” komwe kumasonyeza Mulungu mmaonekedwe amodzi. M’Baibulo, Mulungu amalembedwa kuti ndi Milungu [Elohim] koposa ka 2,500.
Izi zikusonyeza kuti payenera kukhala Mulungu wina, osati “Mulungu Atate” yekha. Mwamuna ndi mkazi analengedwa m’chifanizo cha Mulungu.
“Mulungu [Elohim] adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu [Elohim] adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”Genesis 1:27
Mamuna analengedwa m’chifaniziro cha “Mulungu Atate.” Mkazi analengedwa m’chifanizo cha “Mulungu Amayi.” “Elohim” Mlengi ndi Mulungu Atate ndi “Mulungu Amayi.”
Ndipo zinaloseredwa kuti Mulungu adzaonekera m’masiku otsiriza. (1 Timoteyo 6:15)
Mu nthawi ya Mwana, Mulungu anaonekera ngati Yesu.
M’nthawi ino, Elohim, Mulungu Atate ndi “Mulungu Amayi,” adzabwera kuthupi kudzapulumutsa anthu.
Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse Mpimgo wa Mulungu umakhulupirira Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi monga Mzimu ndi Mkwatibwi-Apulumutsi mu M’badwo wa Mzimu Woyera.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi