Iye amene amapereka madzi a moyo m'mibadwo yonse—nthawi ya Atate, ya Mwana ndi ya Mzimu Woyera, ndi Mulungu yekha.
Komabe, ena amanena kuti oyera mtima akhoza kupereka madzi a moyo. Ndi zopanda pake kuti oyera mtima, omwe amangofikitsa madzi a moyo a Mulungu, anene kuti iwo ndi omwe akupereka madzi a moyo.
Zili ngati munthu wotumiza makalata amene amafikitsa makalata akunena kuti, “Ine ndiye mwini wokupatsani.” Sizikumveka kuchita ngati tikupereka chinachake pamene winawake ndiye akupereka. Ngati tinena kuti ndife amene timapereka china chake chochokera kwa Mulungu, zidzatibweretsera temberero.
Monga anthu a Mulungu, tiyenera kudziwa mtundu wa mawonekedwe omwe Mulungu anabwera kudzatipatsa madzi a moyo m'nthawi ino, chifukwa chake Baibulo limamufotokoza Mulungu ngati Mzimu Woyera ndi Mkwatibwi, komanso momwe akuperekera madzi a moyo.
Mpingo wa Mulungu umakhulupirira mwa Mzimu Woyera Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi amene ndi Mkwatibwi. Tikukhulupirira kuti mudzalandira moyo wosatha kudzera m'madzi a moyo omwe Mulungu Atate ndi Mulungu Amayi akupereka.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi