Masiku ano, mipingo yambiri imati imasunga Pentekoste ndipo amalandira Mzimu Woyera.
Komabe, tikhoza kulandira madalitso a Mzimu Woyera pamene tisunga Pentekoste
pa tsiku limene Mulungu anaika molingana ndi lamulo limene Mulungu anakhazikitsa.
Tsiku la Pentekoste ndi tsiku la 50 kuchokera pa tsiku la zipatso zoyamba [Tsiku la kuuka kwa akufa].
Malinga ndi mawu a Yesu, ophunzirawo anapemphera m’chipinda chapamwamba cha Marko kwa masiku khumi kuchokera pa Tsiku la Kukwera Kumwamba ndipo analandira mzimu woyera pa kusunga Pentekoste.
Mpingo wa Gulu la Utumuki wa Dziko Lonse Mpingo wa Mulungu ndi mpingo wokhawo umene umalandira mdalitso wa Mzimu Woyera woloseredwa m’Baibulo posunga Tsiku la Pentekoste molingana ndi mawu a Yesu.
Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste , anali onse pamodzi pamalo amodzi.
Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Machitidwe 2:1-4
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi