Ntchito Yaikulu ya MulunguYokwaniritsidwa Kudzera muZinthu Zosafunika
Iwo amene ali m'dzanja la Mulungu akhoza kukhala atenga mbali a Ntchito Yaikulu
Mofanana ndi mmene Mulungu anagwiritsira ntchito ndodo ya mbusa kugawa Nyanja Yofiira ndi kupanga akasupe a madzi kuchokera ku thanthwe, chilichonse chimene chili m'dzanja la Mulungu nthawi zonse chimakhala ndi mphamvu yaikulu.
Masiku ano, Mpingo wa Mulungu, umene walandira ntchito yolalikira uthenga wabwino ku Samariya mpaka kumalekezero a dziko lapansi, ukukwaniritsa uthenga wabwino wa padziko lonse kudzera mu mphamvu ya Mulungu, osati ndi khama la munthu aliyense.
Muyeso Omwe Mulungu Amasankha Si Luso, Koma Chikhulupiriro Chathunthu mwa Mulungu
Monga Samisoni amene anagonjetsa Afilisiti chikwi ndi nsagwada ya bulu, monga mnyamata Davide amene anamenya nkhondo ndi chimphona Goliati, ndipo monga Petro, Yohane, ndi Yakobo amene anali asodzi, mu m'badwo uno, amene amakhulupirira Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi ndi chiyembekezo cha ufumu wakumwamba akupanga mbiri yaikulu.
Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu; . . . kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.
1 Akorinto 1:26-29
Nambala ya Owonera94
#Kudalira pa Mulungu
#Mphamvu ya Mulungu
#Kulalikira