Ngati sitimvetsetsa bwino lomwe
dongosolo la Mulungu la
chipulumutso pakuyetsera kuchichita
mwa chifuniro chathu, sitingathe
kulowa mu Kanani wakumwamba
monga Aisrayeli amene
anawonongedwa m’chipululu.
Chifukwa chimene Baibulo limatchulira
Nowa, Abrahamu, Mose, ndi Yoswa
makolo achikhulupiriro ndi chifukwa
chakuti iwo anakhulupirira dongosolo
la Mulungu la chipulumutso ndipo
anachita mogwirizana ndi dongosolo
limenelo.
Uthenga Wabwino wa pangano
latsopano la Mpingo wa Mulungu
unayamba ngati mpingo waung'ono
monga chipinda chapamwamba cha
Marko. Koma malinga ndi dongosolo
la chipulumutso cha anthu limene
Mulungu anakhazikitsa kuyambira
pachiyambi, ukulalikidwa padziko
lonse lapansi, kuphatikizapo Alaska
ndi Sertung kumapiri a Himalaya.
“Ndilalikira za chimaliziro kuyambira
pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale
ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi
kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo
ndidzachita zofuna zanga zonse; . . . inde,
ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza
mtima, ndidzachichitanso.”
Yesaya 46:10-11
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi