Monga momwe salimoni ndi njiwa zingabwerere ku dziko
lakwawo mosasamala kanthu kuti zipita kutali bwanji,
Mulungu anati, “Ndidzaika chilamulo changa m’mitima mwawo,”
ndipo anaika lamulo la pangano latsopano m’mitima ya
anthu kotero kuti iwo abwerere ku mudzi wawo wamuyaya wa kumwamba.
Zaka 2,000 zapitazo, Yesu anafesa
mbewu zabwino [tsiku la Sabata
ndi Paska] kuti apatse
anthu ufumu wakumwamba.
Komabe, mbewu zabwinozo pambuyo pake
zinazimiririka ndipo zinalowedwa m’malo
ndi namsongole, ndiko kuti, malamulo
a anthu ofesedwa ndi mdani, Mdyerekezi.
Ngakhale zili choncho, ana a Mulungu saiwala pangano
latsopano lolembedwa m’mizimu yawo koma amazindikira
ndi mtima wawo, ndipo amabwera kwa Khristu
Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, amene amawatsogolera
ku ufumu wakumwamba, dziko lakwawo la miyoyo yawo.
Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo
ndidzapangana pangano latsopano ndi
nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda; . . .
Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi
nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova;
ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo
m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala
Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;
Yeremiya 31:31-33
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi