Ufumu wawo utakula, mafumu monga Rehobowamu, Saulo,
Uziya, Ahazi ndi Zedekiya anadzikweza n’kuyamba kudzikuza.
Kenako anachimwira Mulungu ndipo anawonongedwa.
Kumbali ina, Yotamu, Davide, Danieli, ndi anzake
atatu anali okhulupirika kwa Mulungu nthaŵi
zonse ndipo anadalitsidwa ndi Mulungu.
Ili ndi phunziro lofunika kwambiri lomwe likuwonetsa
tsogolo la chikhulupiriro chomwe mamembala ampingo
wa Mulungu ayenera kutsatira lero.
Ayenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu nthaŵi zonse,
osati ndi chikhulupiriro chimene chimagwedezeka malinga ndi
nyengo kapena zochitika.
Komanso, ayenera kukhulupirira thandizo la Khristu
Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi ndikugwira ntchito
yolalikira uthenga wabwino molingana ndi mawu
a Mulungu.
Pamenepo, Mulungu adzachititsa Ziyoni kukhala wamphamvu, wokulirakulira,
ndi wolemekezeka pa dziko lonse lapansi monga
mmene ufumu wa Davide unalili.
Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake
analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova
amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira
wobwebweta, kufunsirako,
osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, natembenuzira
ufumu wake kwa Davide mwana wa Jese.
1 Mbiri 10:13-14
Momwemo Yotamu anakulirakulira mphamvu, popeza anakonza njira
zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.
2 Mbiri 27:6
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi