Monga mmene Adamu ndi Heva anatayira ulemerero wa munda wa Edeni chifukwa cha tchimo la kudya zipatso za mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anthu anataya ulemerero wonse chifukwa cha machimo awo kumwamba ndipo anaponyedwa pansi padziko lapansi lino. Anthu analekanitsidwa ndi Mulungu chifukwa cha machimo awo, koma Mulungu anawalola kumulambira Iye kudzera maphwando asanu ndi awiri m’nthawi zitatu, kuphatikizapo tsiku la Sabata ndi Paska, monga njira yokhululukira machimo awo.
Tikhoza titsimikizira m’Baibulo kuti nsembe ya Abele, yomwe inakondweretsa Mulungu, imasonyeza kuti Kristu adzakhululukira anthu machimo mwa kukhetsa mwazi wake pa mtanda. Kudzera mu nsembe ya mwazi, ndiko kuti, kulambira, anthu akhoza kuyandikira kwa Mulungu ndi kukhala mbali ya banja la Mulungu monga ana aamuna ndi aakazi a Kristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, Apulumutsi mu m 'badwo wa Mzimu Woyera.
Koma tsopano mwa Kristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Kristu. . . . Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; Aefeso 2: 13, 19
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi