Nsembe za Chipangano chakale muli kulapa kwa ochimwa ndi chitetezero cha Mulungu. Adamu ndi Hava atachimwa tchimo loyamba, Mulungu analola Kaini ndi Abele kupereka nsembe kupyolera mwa iwo kuti akakwanise kupita ku mtengo wa moyo.
Nsembe inapitira kufikira mu nthawi ya Mose ndipo zinasithidwa kukhala mwambo wopembedza mu nthawi ya Chipangano Chatsopano.
Popanda kupembedza kopereka kwa Mulungu,
chikhululukiro cha machimo sichingapatsidwe.
Mu kupembedza konse mu Chipangano Chakale, nyama zimakhetsa mwazi m'malo mwa ochimwa.
Komabe, mu nthawi ya Chipangano Chatsopano, Yesu Khristu Mwiniwake anaperekedwa monga nsembe yamachimo.
Choncho, tiyenera kusunga mapemphero onse omwe Yesu Khristu adakhazikitsa kudzera mu nsembe Yake, mu mzimu ndi m'chowonadi.
Choondai chakuti Yesu anakhala mkulu wa ansembe, zikusonyeza kuti tiyenera kupitiriza kupereka Mapemphero.
Mamembala a Mpingo wa Mulungu amasunga mapemphero onse monga tsiku la Sabata, Paskha,
ndipo akupita ku chikhululukiro cha machimo ndi chiyembekezo cha Kumwamba chimene Mulungu anatilonjeza.
. . . wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Ahebri 5:9–10
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi