M’buku la Talmud muli nkhani ya mwana amene amazindikira chinsinsi chimene chili m’ chifuniro cha bambo ake n’ kutenga chuma cha bambo ake. Kuti anthu alandire ufumu waulemerero wakumwamba, ayenera kumvetsetsa mawu a Kristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, opezeka m’ mabuku 66 a Baibulo.
Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kulowa m’ Malo Opatulikitsa, koma tsiku limodzi lokha pa chaka. Tsikuli linali Tsiku la Chitetezo. Yesu atamwalira, chinsalu chotchinga cha m’kachisi chinang’ambika ndipo njira yopita ku Malo Oyera Koposa inatsegulidwa.
Kuyambira tsopano, anthu ayenera kupereka uchimo wa imfa umene anachita kumwamba kwa Satana, amene akuimiridwa ndi mbuzi ya Azazele. Ndipo kuti achite chitetezero chamuyaya, ayenera kubwera kwa Mulungu Amayi, amene ali weniweni wa Malo Opatulikitsa.
Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau aakulu, anapereka mzimu wake. Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi;...
Mateyu 27:50-51
Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.
Chivumbulutso 21:22
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi