Kodi n’chifukwa chiyani anthu amakhala moyo waufupi n’kumwalira pamapeto pake?
“Pakuti mphotho yake yauchimo ndi imfa.” Aro 6:23
Baibulo limanena kuti chifukwa chimene tiyenera kufa ndichifukwa cha machimo athu. Ngati machimo athu oyenera imfa akhululukidwa. Ngakhale matupi athu awonongeka, mizimu yathu ikhoza kukhala ndimoyo kosatha. Ndiye, tingalandire bwanji chikhululukiro cha machimo?
“Yohane (M’batizi) anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wakutembenuka mtima wakuloza kuchikhululukiro cha machimo. Ndipo anatuluka a kudziko lonse la Yudeya, ndi a kuYerusalemu onse; nadza kwaiye nabatizidwa ndi iye mumtsinje wa Yordani, powulula machimo ao.” Mrk 1:4~5
Yesu anadutsa mu ubatizo, njira yakuchikhululukiro cha machimo, kutipasa ife chitsanzo. (Mat 3:13) Ubatizo ndi mwambo woyera umene tingalandire nawo Chikhululukiro cha machimo ndikubadwanso monga ana a Mulungu.
Ngati ndichoncho, kodi tiyenera kubatizidwa liti?
Pamene tazindikira Khristu, tikuyenera kubatizidwa. (Mac 16:13-15)
Anthu amabatizidwa angakhale pa msewu. (Mac 8:27-38) komanso pa ola lapakati pa usiku. (Mac 16:25-33)
Chifukwa chiyani makolo athu achikhulupiriro anabatizidwa Pompopompo pamene iwo anazindikira Khristu? Zinali choncho chifukwa anakhulupirira lonjezo la Mulungu loti moyo wawo udzakhala kosatha ngakhale matupi awo awonongeka ngati alandira chikhululukiro cha machimo kudzera mu ubatizo. Ndichifukwa chake ubatizo umachitika m’dzina la Mpulumutsi amene alindiulamuliro wakukhululukira machimo, ndikupereka moyo wosatha. (Mat 28:19)
Kodi mukudziwa dzina la Mpulumutsi-dzina la Atate, la Mwana, ndi la Mzimu Woyera?
Dzina la Atate ndi Yehova, ndipo dzina la Mwana ndi Yesu. Ndiye dzina la Mzimu Woyera ndindani?
Iwo amene abatizidwa mu dzina la Yehova, la Yesu ndi la Ahnsahnghong—dzina latsopano la Yesu ndi Mpulumutsi mu Mbado wa Mzimu Oyera—atha kulandira chikhululukiro cha machimo ndi moyo wosatha. (Chiv 3:12)
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi