Monga momwe anthu onse padziko lapansi
ali ndi ntchito zawo, ana a Mulungu
amene abadwa mu nthawi ya Mzimu Woyera
amapatsidwa ntchito ya atumiki wa pangano latsopano,
asodzi a anthu, alonda, ndi mboni za Mulungu.
Mulungu amapereka ntchito yapadera kwa anthu
amene amawakhulupirira ndi kuwaona ngati olungama.
Ndiye kuchitira umboni za Mulungu amene
anabwera ku dziko lapansi m’thupi monga
momwe anachitira mtumwi Paulo.
Monga mboni za Mulungu, mamembala a mpingo
wa Mulungu amachitira umboni ndi mitima
yawo yonse za Khristu Ahnsahnghong ndi
Mulungu Amayi amene anabwera ngati Apulumutsi
mu m’badwo wa Mzimu Woyera kuti athe
kuyenda m’njira yachikhulupiriro popanda kunong’oneza bondo.
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera
atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni
zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya
monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira
malekezero ake a dziko.
Machitidwe 1:8
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi