Munthu aliyense wobadwira padziko lapansi pano, monga Solomoni ndi Yobu, anali mngelo amene anakhalako mu ufumu wa kumwamba. Timaphunzitsidwa kuti moyo padziko lapansi pano ndi wodzaza ndi mavuto ndi chisoni chifukwa ndi malo amene angelo, omwe kale ankakhala mu ulemerero ndi Mulungu kumwamba, anaponyedwako atachita tchimo lalikulu limene limatsogolera ku imfa.
Lero, Amene wabwezeretsa Paska wa pangano latsopano wotayika si wina koma Mulungu wathu. Izi zili choncho chifukwa Paska wa pangano latsopano ndi pangano limene Yesu anakhazikitsa kudzera mu nsembe yake pamtanda, kuti anthu onse machimo awo amene anachita kumwamba, amene amatsogolera ku imfa, akhululukidwe ndipo abwerere ku ufumu wa kumwamba.
Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake... Aefeso 1:7
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. Aroma 6:23
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi