Monga Akhristu, tiyenera kukhala mchere ndi kuwala kwa dziko pamene tikukhala moyo wathu. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu anatipatsa chiphunzitso chakuti: “Khalanibe achangu pa zinthu zauzimu, potumikira Mulungu. Khalani okondwa m’chiyembekezo, oleza mtima m’chisautso, ndi wokhulupirika m’mapemphero. Khalani ochereza. Gawanani ndi anthu a Mulungu omwe ali osowa. Kondanani wina ndi mnzake ndi kulemekezana wina ndi mnzake koposa inu nokha.”
Christ Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi anati pamene tizindikira chisomo cha chikhululukiro cha machimo ndi chipulumutso choperekedwa ndi Mulungu ndikugawana ndi ena, ndiko kukwaniritsidwa kwa lamulo la m’Baibulo. Akristu oona ayenera kusonyeza chikondi cha Mulungu ndi mtima womwewo.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Aroma 12:1–2
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi