Mulungu anaphunzitsa Aisiraeli kusunga malamulo ake monga
tsiku la Sabata m’chipululu kotero kuti akathe
kusunga malamulo a Mulungu ku Kanani.
Chimodzimodzinso, Mulungu amalola iwo amene akuyembekezera ufumu
wakumwamba kuphunzira chilankhulo chakumwamba, chimene chiri chilankhulo
cha chikondi, chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chipulumutso, m’moyo
wawo wa tsiku ndi tsiku asanalowe mu
ufumu wakumwamba.
Anthu olankhula chilankhulo chakumwamba analandira madalitso a Mulungu.
Yoswa ndi Kalebe analowa m’dziko la Kanani,
ndipo anzake atatu a Danieli anatetezedwa ku
ng’anjo ya lawi la moto.
Momwemonso, amene amalankhula chilankhulo chakumwamba molingana
ndi ziphunzitso za Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi
akhoza kulowa mu ufumu wamuyaya wakumwamba.
Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.
Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu
wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse. . . . Ndipo lilime
ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa
ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi
lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa
ndi Gehena.
Yakobo 3:2-6
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi