98% ya zimene timalankhula zimalembedwa mu ubongo wathu. Pamene ndemanga yoipa yalembedwa mu ubongo wathu,pamafunika ndemanga chikwi zabwino kuti zifafanize ndemanga imodzi yoipayo. Mulungu anatiuza kuti nthawi zonse tizilankhula zinthu zabwino pakupereka mayamiko pakukhala okondwera kuti tithe kuzindikira kufunika kwa Kumwamba ndi kusunga madalitso Kumwamba.
Mamembala a Mpingo wa Mulungu ndi anthu amene anazindikira kufunika ndi dalitso la Kumwamba. Iwo ndiwo amene amalalikira uthenga: “Tiyeni tilandira mpumulo wosatha pakusunga tsiku la Sabata ndi moyo wosatha pakusunga Pasika. Komanso, tiyeni tikhale ana a Mulungu polandira Atate Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi.” Iwo nthawi zonse amaganizira ulemerero wosatha wa Ufumu wa Kumwamba, osati ulemerero wa dziko lino omwe udzapita m’kuphethira kwa diso.
Chifukwa chake sitifooka . . . Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero.Popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka.Pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
2 Akorinto 4:16–18
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi