Ufumu wakumwamba ndi malo
a kukondwa kosatha ndi chisangalalo,
kopanda imfa, ululu, kapena kuvutika.
Ichi ndichifukwa chake Mulungu
adatiuza kuti tisakhale ndi moyo
wopanda cholinga ngati kuti tikhala ndi zaka
chikwi pomwe sitingathe kukhala ndi zaka
zana, koma kukhala ndi moyo
chifukwa cha ufumu wakumwamba.
Monga Yesu anapatsa anthu moyo kudzera mu Paska
wa pangano latsopano zaka 2,000 zapitazo, Khristu
Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi atiphunzitsa
kuti tiyenera kusunga Paska kuti tikhale ndi moyo
wosatha, osati moyo umene umafota
ngati maluwa akuthengo.
Pakuti masiku athu onse apitirira
mu ukali wanu; titsiriza moyo
wathu ngati lingaliro.
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu
ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi
zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula
kwao kumati chivuto ndi chopanda pake;
pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Masalimo 90:9–10
Popeza, Anthu onse akunga udzu,
ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu.
Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;
koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. . . .
1 Petro 1:24-25
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi