Kutengera zomwe zilimo, botolo
lopanda kanthu limatha
kukhala botolo la duwa
kapena botolo lamadzi.
Monga momwe atumwi anakhala antchito a
pangano latsopano atalandira Mzimu Woyera
pa tsiku la Pentekoste zaka 2,000 zapitazo,
ifenso tikhoza kukhala ana angwiro a Mulungu
tikakhala ndi Mzimu Woyera mwa ife.
Zaka 2,000 zapitazo, Yesu atafa pamtanda,
atumwi anali kunjenjemera ndi mantha,
koma atalandira mzimu woyera pa Tsiku
la Pentekosite, anachitira umboni
molimba mtima kuti Yesu ndi Mesiya.
Monga momwe atumwi anachitira, mamembala a Mpingo
wa Mulungu lero, atalandira Mzimu Woyera wa mvula
ya masika pa Tsiku la Pentekoste, akuchitira
umboni molimba mtima kuti Khristu Ahnsahnghong
ndi Mulungu Amayi abwera kudzapulumutsa anthu.
Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste ,
anali onse pamodzi pamalo amodzi.
Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau
ochokera Kumwamba ngati mkokomo
wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba
yonse imene analikukhalamo. . . .
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu
Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime
ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Machitidwe 2:1-4
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi