Tiyenera kufunafuna Mulungu chifukwa mayankho amavuto
m’miyoyo yathu amaperekedwa ndi Mulungu
nthawi zonse.
Chifukwa chimene Davide, Yehosafati, ndi Hezekiya
anakhala ndi moyo wodalitsika ndi wopambana
chinali chakuti iwo ankadalira Mulungu, osati
anthu kapena zinthu za m’dzikoli.
Mulungu analemba mbiri yakale m’Baibulo kwa
ife amene tikukhala mu nthawi ino.
Nthaŵi zonse Mulungu anali ndi anthu
ake—pamene Yeriko analandidwa ndipo Nyanja
Yofiira inagawika.
Pokumbukira izi, mamembala a Mpingo
wa Mulungu nthawi zonse amadalira Mulungu
pamavuto awo onse.
Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse
nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika,
pamaso pa Yehova Mulungu wake.
Ndipo m’ntchito iliyonse anaiyamba mu
utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi
m’chilamulo, ndi m’mauzo, kufuna Mulungu wake,
anachita ndi mtima wake wonse,
nalemerera nayo.
2 Mbiri 31:20-21
Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa
Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo
wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda;
nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse
kuyambira pomwepo.
2 Mbiri 32:23
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi