Njira yopulumukira masoka ndiyo kusunga Paskha wa Pangano Latsopano. Mpingo wa Mulungu wokha, umene unakhazikitsidwa ndi Khristu Ahnsahnghong amene anabwera kachiwiri monga momwe Baibulo linanenera, ndi womweumasunga Paskha wa pangano latsopano molingana ndi ziphunzitso za Baibulo.
Kusintha kwa nyengo, zivomelezi, mphepo yamkuntho, njala, ndi nkhondo zikupitirirabe, ndipo kuphana sikukutha. Ngati zionongeko zimenezizikugwerani, kodi mungathe kuzipewa?
Nkhondo! Njala! Zivomelezi! Miliri ya matenda!
Anthu amene anataya ana awo akulira, akutchula mayina awo. Anthu ovala nsanza ndi njala amadya zotoledza pansi ndi kulira mwakachetechete. Tonsefe tikunjenjemera chifukwa cha mantha a kusintha kwa nyengo, zivomelezi, mphepo yamkuntho, nkhondo, ndi njala, Miliri ya matenda, yomwe ingatigwere nthawi iliyonse.
Chonde imvani kubuula kwathu zionongekozi! O Mulungu Wamphamvuyonse, amene anatulutsa Aisrayeli muzionongeko kudzeramu Paskha! Chonde tichitireni chisoni ndipo mutidziwitse njira yopulumukira ku zionongekozimenezi! Chonde tipulumutseni!
Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, pamene tsoka lalikulu lopha ana oyamba kubadwa linafika pa Igupto, mabanja amene anachita Paskha pa kupha ana a nkhosa achaka chimodzi ndi kupaka magazi m’mbali ndi pamwamba pa mafelemu a zitseko, sanavulazidwe mwanjira iriyonse.
“ ‘Ndipomwaziwoudzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndionamwaziwondidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko laEjipito. . .’ ” Eks 12:11-14
Paska, chizindikiro cha mphamvu ya Mulungu, imatiteteza ku zionongeko! Paska amene anali ku Iguputo anali mthunzi. Paskha, amene Yesu anakhazikitsa asanapachikidwe, ndiyezenizeni zake. (Luk 22:20; Mat 26:17)
Paska wa pangano latsopano, amene tingatenge nawo mbali m’mwazi wamtengo wapatali wa Yesu, ayenela kusungidwanso m’nthawi ino. Komabe, pa Msonkhano wa ku Nicaea umene unachitika mu AD 325, Paskha wa pangano latsopano, amene mwanziwamtengo wapatali wa Yesu analonjezedwa, anathetsedwa kotheratu.
Chosangalatsa n’chakuti Mulungu ananena kuti: “Pa nthawi yake ndidzachita zimenezi mofulumira.” (Yes 60:22), Ndipo nthawi yafika yoti anthu achite Paska, yomwe ndi choonadi cha Mulungu, yaululidwa. Khristu Ahnsahnghong amene anabwera kachiwiri monga momwe kunanenedwera m’Baibulo wabwezeretsanso Paskha wa pangano latsopano.
“Padziko lonse lapansi, ndi Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse wa Mpingo wa Mulungu (Mbusa wankulu Kim Joo-cheol) omwe amakondwerera Paskha ndi mkate komanso vinyo ngati Mgonero Womaliza wa Yesu Khristu.”
O Mulungu, tiloreni tilalikire Paska wa pangano latsopano, njira yokhayo yotenga nawo mbali m’mwazi wamtengo wapatali wa Yesu, kuti dziko lonse limusunge ndi kupulumutsidwa ku zionongeko!
Chonde bwerani ku Mpingo wa Mulungu, womwe unakhazikitsidwa ndi Khristu Ahnsahnghong yemwe anabwera kachiwiri molingana ndi maulosi a m'Baibulo, ndikusunga Paska wa pangano latsopano, ndipo mudzapulumutsidwa ku zionongeko ndi kulandira moyo wosatha.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi