Mulungu anatchula mpingo umene
umasunga zikondwerero zake Ziyoni.
Mpingo wokhawo umene
umasunga zikondwerero za Mulungu
olembedwa m’Baibulo—Sabata,
Paska, Chikondwerero cha Mikate Yopanda
Chotupitsa, Chikondwerero cha Zipatso
Zoyamba, Tsiku la Pentekoste,
Chikondwerero chaMalipenga, Tsiku la
Chitetezo, ndi Chikondwerero cha Misasa—
ndi Mpingo wa Mulungu.
Yesu anakhazikitsa pangano
latsopano ndi magazi ake amtengo
wapatali, osati ndi magazi a nyama
malinga ndi Chilamulo cha Mose.
Anatiphunzitsanso kuti malo amene
zikondwerero za pangano latsopano
zimachitikira ndi Ziyoni kumene
chipulumutso cha anthu
chimaperekedwa.
Komabe, zikondwerero za pangano
latsopano zinazimirira mkati mwa
Nyengo Yamdima, ndipo Ziyoni
anawonongedwa.
Lero, Khristu Ahnsahnghong
anamanganso Ziyoni yomwe inali
itawonongedwa.
Pakuti Yehova anamanga Ziyoni, anaoneka
mu ulemerero wake;
Salmo 102:16
Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa
zikondwerero zathu; maso ako adzaona,
Yerusalemu malo a phee, chihema chimene
sichidzasunthidwa, . . . Koma pamenepo
Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero . . .
Yehova ndiye mfumu yathu; Iye
adzatipulumutsa.
Yesaya 33:20-22
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi