Pamene Mulungu anasankha gulu lankhondo la Gideoni, Iye adakana amene adali ndi mantha.
Iye nthawizonse anatsimikizira a ankhondo a Yoswa kuti asakhale ndi mantha.
Kupyolera mu izi, tikhoza kuona kuti chofunika kwambiri ndikukhulupilira
malonjezo a Mulungu ndi kupita patsogolo ndi kulimba mtima.
Monga Aisiraeli amene sanakhulupirire Mmalonjezo a Mulungu, anafalitsa mbiri yoipa,
ndipo anadandaula za Kanani, ngati ife tichita mantha chifukwa timaopa anthu
ndi zotizungulira, sitidzakhala okhoza kulowa mu Ufumu wa Kumwamba
Kanani wauzimu. Tikamalalikira molimba mtima Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Kumwamba,
kukhulupirira lonjezo limene Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi anatipatsa
Kuti atidalitse, ntchito yodabwitsa ya uthenga wabwino yomwe idzadabwitsa dziko lonse lapansi idzachitika.
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako;
koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti
usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo;
popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu,
nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa,
pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
Yoswa 1:8–9
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi