Atasangalala ndi zinthu zonse zimene anthu
a m’dzikoli ankalakalaka, Solomoni pomalizira pake
anafika potsimikiza kuti chilichonse cha
padziko lapansi n’chachabechabe, kungothamangitsa
mphepo, ndiponso kuti anthu ayenera kuopa
Mulungu ndi kumvera mawu Ake kuti alandire madalitso.
Mulungu amadalitsa amene amasunga malamulo ake,
ndipo amawakweza pamwamba pa mitundu yonse.
Monga momwe Mfumu Hezekiya ndi Yosiya
ya kummwera kwa Yuda adadalitsidwa chifukwa
chomvera mawu a Mulungu, Mpingo wa Mulungu
umatamandidwa ndi kukwezedwa padziko lonse
lapansi chifukwa chogwiritsa ntchito ziphunzitso
za Khristu Ahnsahnghong ndi Amayi akumwamba.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova
Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita
malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti
Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa
amitundu onse a padziko lapansi;
ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi
kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu. . . .
Deuteronomo 28:1-2
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi