Monga momwe Abraham Lincoln
anaunikira asilikali pankhondo
yachiweniweni ya ku America,
ngati tipemphera kwa Mulungu
kuti, “Chonde mukhale kumbali
yanga,” sitingadziŵe ngati tili
panjira yolondola kapena yolakwika.
Choncho, kuti tipulumuke, tiyenela
kupemphera kuti, “Chonde
ndikhale kumbali ya Mulungu nthawi zonse.”
Eliya anakumana ndi aneneri
onyenga 850, ndipo anzake atatu
a Danieli sanagwadire fano lagolide.
Abrahamu anakhala kholo la
chikhulupiriro, ndipo Nowa
anatchedwa wolowa nyumba wa chilungamo.
Anthu amenewa nthawi zonse
anali ku mbali ya Mulungu.
Momwemonso, mu nthawi ya
Mzimu Woyera, mamembala a
Mpingo wa Mulungu, omwe
amakhulupirira Mulungu
Ahnsahnghong ndi Mulungu
Amayi, amapemphera kuti nthawi
zonse azikhala kumbali ya
Mulungu muzochitika zilizonse
zomwe zingachitike panjira yachikhulupiriro.
Chifukwa chake khalani akutsanza a
Mulungu, monga ana okondedwa;
ndipo yendani m'chikondi monganso
Khristu anakukondani inu, . . .
Aefenso 5:1-2
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi