M’nthawi ya Chipangano Chakale, Malo Opatulikitsa amene anali kusunga Likasa la Chipangano anali ndi utali wofanana, m’lifupi, ndi msinkhu wake.
Mzinda Woyera wa Yerusalemu wakumwamba umene uli waukulu ndi wautali monga mmene unalili wautali ukuimira Mkwatibwi, Mulungu Amayi. Iye ndiye gwero la madzi a moyo ndi chenicheni cha Malo Opatulikitsa.
Monga mmene Mulungu analengera kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi mawu ake pachiyambi, tiyenera kukhulupirira kuti mawu akuti, “Landirani Mzimu Woyera,” operekedwa pa Tsiku Lomaliza la Phwando la Misasa alinso ndi mphamvu.
Pamene tilalikira uthenga wabwino ndi chikhulupiriro ichi, ntchito ya Mzimu Woyera wa mvula ya masika yomwe ili yamphamvu kwambiri kuposa ntchito ya Mzimu Woyera yomwe inakwaniritsidwa mu mpingo woyamba idzachitika.
Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa....nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,...ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.
Chivumbulutso 21:9-16
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi