Palibe m’modzi mwa anthu ambiri a dziko lapansi amene angalungamitsidwe ndi Mulungu kapena kulandira chipulumutso kapena chikhululukiro cha machimo kapena lonjezo lakukhala ansembe achifumu akumwamba pokhapokha atachita nawo Paskha wa Pangano Latsopano limene Yesu anakhazikitsa ndi mwazi wake wokhetsedwa pa mtanda.
Popeza sitingakhale ndi moyo popanda kudya ndi kumwa thupi ndi mwazi wa Mulungu, Khristu Ahnsahnghong anabwera kachiwiri, nabwezeretsa Paskha amene anathetsedwa mu AD 325, ndipo anachitira umboni za Yerusalemu Mayi wa Kumwamba, gwero la moyo kwa anthu.
podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: 19koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu.
1 Petulo 1:18–19
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
Yohane 6:53
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi