Tsiku lopembedza Mulungu ndi Sabata la tsiku lachisanu ndi chiwiri, lomwe ndi Loweruka pakati pa masiku a sabata. Sabata ndi tsiku lopatulika lolonjezedwa ndi madalitso, ndipo ndi tsiku loti anthu adziwike kuti ndife anthu a Mulungu. Monga lamulo lachinayi la Malamulo Khumi, ndi tsiku la kulambira limene anthu ayenera kusunga. Ndicho chifukwa chake Yesu, Khristu Ahnsahnghong, ndi Mulungu Amayi anapereka chitsanzo cha kusunga Sabata.
N’chifukwa chiyani Mulungu anakana nsembe ya Kaini ndipo anangolandira nsembe ya Abele? N’chifukwa chiyani Mulungu anawononga ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, amene anali ansembe, amene masiku ano ndi abusa? Zinali choncho chifukwa anachita zinthu mogwirizana ndi maganizo awo ndipo sanamvere mawu a Mulungu. Momwemonso, kulambira Mulungu mwa kusunga Sabata mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndicho chinsinsi chachikulu cha madalitso.
Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo . . .
Genesis 2:3
“Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika.”
Eksodo 20:8
Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m’sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m’kalata.
Luka 4:16
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi