Popanda kusunga malamulo a Mulungu, sitingathe kudziwa Khristu, chinsinsi cha Mulungu. Ndi chifukwa chakuti Mulungu amapereka chidziwitso kwa okhawo amene amasunga malamulo a Mulungu monga Sabata ndi Paska ya Pangano Latsopano kuti athe kuzindikira Mulungu amene wabwera m’thupi.
Iwo amene amasunga malamulo opangidwa ndi anthu amatenga Sabata ndi Paska ngati zosafunikira, koma iwo amene alandira chidziŵitso kuchokera kwa Mulungu amazindikira tanthauzo lenileni la lamulo lirilonse la Mulungu nafuula kuti, “Uyu ndiye Mulungu wathu,” monga momwe Yesaya analoserera. Kristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, amene awononga imfa pakubwezeretsa Paska imene sinakondweredwe kwa zaka zoposa 1,600, ndiwo Milungu yowona Imene anthu akhala akuiyembekezera kwa nthaŵi yaitali.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho
chidziwitso chokoma.Chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Masalimo 111:10
Ndipo m’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe … Iye wameza imfa kunthawi yonse … Ndipo adzanena tsiku limenelo, “Taonani uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa.”
Yesaya 25:6–9
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi