Kulambira kwa lamlungu ndi Khrisimasi ndizopembedza mulungu dzuwa, ndipo ndi za malamulo a anthu. Yesu mu M’badwo wa Mwana, ndi Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi M’badwo wa Mzimu Woyera adatiphunzitsa kuti iwo omwe amasunga malamulo aanthu ndi aneneri onyenga posatengera m’mene amawonekera kunja.
Aneneri onyenga amadzionetsa okha ngati abusa abwino monga mimbulu yovala zovala za nkhosa. Komabe, amapusitsa anthu kotero kuti anthu amalephera kusunga malamulo omwe Mulungu watilamula kuti tisunge.
Mpingo wa Mulungu wokha ndi malo omwe ana amkazi amasunga malamulo a Mulungu monga Tsiku la Sabata ndi Paskha ndikusiyanitsa chowonadi ndi bodza.
Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
Mateyu 15:7–9
Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwao ali mimbulu yolusa
Mateyu 7:15
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi