Monga momwe oyera mtima a Mpingo woyambirira
anali ndi chiyembekezo cha chiukitsiro mwa kuuka
kwa Yesu Khristu ndipo sanaope zovuta, mazunzo,
kapena mikhalidwe yoipa ya dziko lino,
momwemonso oyera mtima a Mpingo wa Mulungu.
Iwo samangokhalira kukhalira moyo zinthu
zooneka ndi maso kapena za kanthawi kochepa,
koma amakhala ndi chiyembekezo cha kuuka
kwa akufa chakuti adzakhala ndi
matupi auzimu m’dziko lauzimu.
Yesu ataukitsidwa, mwadzidzidzi anazimiririka
pamene anali kukambirana ndi ophunzira ake,
mosayembekezereka anawonekera m’chipinda
chotsekedwa, ndi kusonyeza kukwera
kwake kumwamba pamaso pawo.
Izi zikusonyeza kuti ifenso, tidzakhala
ngati Yesu m’mawa wa chiukitsiro.
Palinso matupi am'mwamba, ndi
matupi apadziko: koma ulemerero
wa lam'mwamba ndi wina, ndi
ulemerero wa lapadziko ndi winanso. . . .
Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.
1 Akorinto 15:40-44
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi