Mpingo wa Mulungu umasunga maphwando monga tsiku la Sabata ndi Paskha,
amene ali malamulo a Mulungu.
Ngati sitisunga malamulo a Mulungu, sitingalandire nzeru yabwino, ndipo nzeru zathu
ndi luntha lathu zimachoka, zomwe zimatitsogolera kuchita zoipa pokhulupirira kuti kulibe Mulungu.
Baibulo likuchitira umboni kuti iwo amene amafunafuna Yehova mu m’badwo wa Atate,
Yesu Khristu mu m’badwo wa Mwana, ndi Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi—
Mzimu ndi Mkwatibwi—mu m’badwo wa Mzimu Woyera
ndi amene ali ndi luntha. monga anthu oona a Mulungu ndipo adzapulumutsidwa.
Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.
Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone
ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Onse anabwerera; anavunda mtima pamodzi;
palibe mmodzi wakuchita bwino, nnena mmodzi.
Masalimo 53:1-3
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru;
onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma;
chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Masalimo 111:10
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi