Ngakhale wochimwa atayiwala tchimo
lake ndi kukhala ndi moyo watsopano,
tchimo lake silitha.
Anthu ndi akaidi osaweruzidwa omwe
anachimwa kumwamba ndipo
akuyembekezera chiweruzo
chakumwamba kapena kugahena.
Pambuyo pa mwayi womalizira wolapa
padziko lapansi lino kudzera m’
chilamulo cha pangano latsopano, iwo
ayenera kuima pamaso pa mpando wa
chiweruzo wa Mulungu, ndipo
adzapatsidwa chiweruzo chomaliza cha
machimo awo.
Lamulo la pangano latsopano lili ndi
lonjezo lochotsa machimo athu onse
ndi zolakwa zathu.
Yesu anazunzika pa mtanda kuti
achotse machimo aakulu a ochimwa
auzimu. Khristu Ahnsahnghong ndi
Mulungu Amayi adabwezeretsa lamulo
la pangano latsopano lomwe lili ndi
chisomo chotere cha chiombolo.
Monga mmene Yesu anachitira, Iwo
akufuula mowona mtima kuti, “Lapani”
ndi kutsogolera anthu ku ufumu
wakumwamba.
Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa
kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;
Ahebri 9:27
Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa
m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri,
ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu
sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo,
anaponyedwa m'nyanja yamoto.
Chivumbulutso 20:14-15
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi