Tikayang’anitsitsa zozizwitsa zimene zinachitika m’Nthawi ya Atate komanso mu Nthawi ya Mwana monga mmene Mulungu anagawawira Nyanja Yofiira, kugwetsa mzinda wa Yeriko, ndi kuimitsa dzuwa, tingathe kumvetsa kuti chilichonse chidachitika molingana ndi mawu a Mulungu.
Mulungu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi anabwera ku dziko lapansi ngati Mzimu ndi Mkwatibwi mu Nthawi ya Mzimu Woyera. Nthawi zonse tikamvera mawu a Mulungu, kukhulupirira kuti ntchito ya uthenga wabwino imakwaniritsidwa ndi Mulungu, ntchito yodabwitsa ya uthenga wabwino ikuchitika ngakhale pakali pano.
(Fungo la Ziyoni: Ntchito ya uthenga wabwino yomwe inakwaniritsidwa m’miyezi inayi pambuyo pa chikondwerero cha kulalikira cha Pentekosite)
Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova, tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele . . . : ndipo anati pamaso pa Israele, “Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m’chigwa cha Ayaloni.” Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima, mpaka anthu adabwezera chilango adani ao.
[Yoswa 10:12–13]
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse naumitsa Nyanja. Ndipo madziwo anagawikana.
[Eksodo 14:21]
Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, “Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.” . . . “Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu. Koma pa mau anu ndidzaponya makoka.” Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba ndipo makoka ao analinkung’ambika;
[Luka 5:4–6]
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi