Oyera mtima a Mpingo
woyamba anapemphera mowona mtima
kwa masiku khumi kuchokera
pa Tsiku la Kukwera
Kumwamba kufikira pa Tsiku
la Pentekosti. Pa Pentekosti,
analandira Mzimu Woyera umene
unawalola kukhala ndi chikhulupiriro
cholimba ndi kufalitsa uthenga
wabwino mofulumira. Mu nthawi
ya Mzimu Woyera, Mulungu
amatipatsa ife mphatso za
Mzimu Woyera pa Pentekosti,
ngakhale kuwirikiza kasanu ndi
kawiri kuposa zaka
2,000 zapitazo.
Atalandira Mzimu Woyera, Mpingo
woyamba unachitira umboni, “Yesu
ndiye Khristu.” Momwemonso, tsopano
mamembala a Mpingo wa
Mulungu, amene analandira Mzimu
Woyera wa mvula ya
masika atasunga Pentekosti, ndi
kulalikira molimba mtima ku
dziko lapansi Apulumutsi athu,
Khristu Ahnsahnghong ndi Amayi
a Kumwamba.
Ndipo pakufika tsiku la
Pentekoste , anali onse pamodzi
pamalo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi
anamveka mau ochokera Kumwamba
ngati mkokomo wa mphepo yolimba,
nadzaza nyumba yonse imene
analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa
iwo malilime ogawanikana, onga
amoto; ndipo unakhala pa
iwo onse wayekhawayekha. Ndipo
anadzazidwa onse ndi Mzimu
Woyera, nayamba kulankhula ndi
malilime ena, monga Mzimu
anawalankhulitsa.
Machitidwe 2:1-4
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi