Kupyolera m’fanizo limene Yesu anatipatsa, timafika pozindikira kuti
Abrahamu akuimira Mulungu Atate, ndi kuti Sara, amene anachita mbali
yofunika kwambiri posankha olowa m’nyumba a m’banja la Abrahamu,
ndi Amayi wathu, amene ali mfulu ndipo akuimiridwa ngati pangano latsopano.
Iwo amene sakhulupirira konse mwa Mulungu monga Eliezere,
amene makolo ake anali akapolo, kapena amene amangokhulupirira mwa
Mulungu Atate, monga Ismayeli, sangakhale olowa nyumba a Mulungu.
Monga Isake, iwo amene alandira Mulungu Atate (Christ Ahnsahnghong)
ndi Mulungu Amayi, amene ali mfulu, ndipo asindikizidwa monga,
“Ana Anga,” kupyolera mu thupi ndi mwazi wa Mulungu,
akhoza kukhala olowa nyumba a ufumu wakumwamba.
“Munthu wolemera uja anamwaliranso ndipo anaikidwa m’manda.
Mu gehena, kumene anali kuzunzika, anakweza maso ake,
nawona Abrahamu patali, ndi Lazaro pambali pake.
Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo …”
Luka 16:22–24
Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye
wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo
zophiphiritsa, … abale, sitili ana a mdzakazi, komatu a mfulu.
Agalatiya 4:23–31
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi