Mulungu amati, “Musaonjezera kapena
kuchotsapo pa mawu a m’Baibulo,” ndipo
m’Baibulo munalembedwa kuti anthu
atha kupulumutsidwa ngati apita kwa Mzimu ndi
Mkwatibwi, amene amapereka madzi a moyo.
Chotero, Mpingo wa Mulungu, umene
umakhulupirira mwa Mulungu Mzimu
Woyera, Khristu Ahnsahnghong, ndi Mulungu
Amayi, amene ali Mkwatibwi, ndi mpingo
umene Mulungu amakondwera nawo ndipo
umene udzapulumutsidwa.
Mtumwi Paulo analemba m’Baibulo kuti ana
a lonjezo ndiwo otsalira osankhidwa mwa
chisomo ndipo amene adzapulumuke ndi ana
a lonjezo ngati Isake. Zikutanthauza kuti iwo
amene akhulupilira mwa Mulungu Amayi mu
nthawi ya Mzimu Woyera adzakhala ana a
lonjezo monga Isake ndi otsalira osankhidwa
ndi chisomo cha Mulungu kuti apulumutsidwe.
Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a
lonjezano.
Agalatiya 4:28
Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti,
Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala
monga mchenga wa kunyanja, chotsalira
ndicho chidzapulumuka.
Aroma 9:27
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi