Alexander Wamkulu, amene anagonjetsa gawo limodzi mwa magawo anayi a dziko lapansi ndipo anthu ankamulemekeza kwambiri, nayenso anamaliza moyo wake pachabe. Ngakhale munthu ali nazo zonse zapadziko lapansi, ngati sadziwa za dziko lamuyaya, moyo wake umakhala wopanda tanthauzo.
Chuma, ulemu, ndi mphamvu za dziko lapansili sizikhalitsa, koma ndi zopanda ntchito pakukumana ndi imfa.
Choncho Khristu Ahnsahnghong anatiuza kuti tikonzekere dziko lauzimu kumene kuli chisangalalo chosatha.
Ndichifukwa chakuti chofunikira chenicheni chathu si thupi lathu koma mzimu wathu (Yohane 6:63).
Moyo wopanda kudziwa za dziko lamuyaya ndi wopanda tanthauzo.
Moyo wathu waufupi padziko lino lapansi ndi nthawi yokonzekera dziko lamuyaya.
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipite kudziko lauzimu lamuyaya?
Dziko lauzimu lamuyaya lopanda ululu kapena imfa, (Chivumbulutso 21:4) thupi lochivundi silingalowe, koma yekhayo amene ali ndi moyo wosatha angathe kulowa. (1 Akorinto 15:50)
Ndiye, tingakhale bwanji ndi moyo wosatha?
Tikadya thupi la Yesu ndi kumwa mwazi wake tikhoza kukhala ndi moyo wosatha. (Yohane 6:54)
Yesu analonjeza kuti mkate ndi vinyo wa Paska ndi thupi ndi mwazi wake.(Mateyu 26:26)
Choncho, amene adzalandire moyo wosatha kudzera mu Paska akhoza kulowa m’dziko lauzimu, kumene adzayende momasuka m’yunivesi yonse. Tiyeni tiyang’ane chitsogolo ku dziko lauzimu lamuyaya, m’malo mowononga moyo wathu, kungoyang’ana zinthu zakuthupi, ndi kutenga nawo mbali mu lonjezo lopatulika la moyo wosatha [Paska].
Mpingo wa Mulungu umene Khristu Wobwera Kachiwiri Ahnsahnghong anakhazikitsa ndi mpingo wokhawo umene umatsatira Pangano Latsopano la Paska.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi