Khristu Ahnsahnghong ananena kuti ngati
sitichita choonadi, mizimu yathu
idzadetsedwa ndi kutaya kuzindikira ndipo
pamapeto pake, kutaya chikhulupiriro ndi kukana Mulungu.
Popeza tikukhala padziko lino lapansi, dziko
la ngodya zitatu, ndipo sitingathe kuweruza
dziko lakumwamba mu ngodya zinayi ndi zisanu,
tiyenera kukhulupirira mawu a Mulungu amene
amatidalitsa nthawi zonse ndi kutsatira chiphunzitso chake.
Makolo akale achikhulupiriro onga Mose,
Davide, Gidiyoni, ndi Yoswa anadalitsidwa mwa
kumvera mawu a Mulungu ngakhale mu nyengo
imene inawoneka kukhala yosatheka
m’kulingalira wamba kwa anthu.
Kuyang’ana mbiri yawo, mamembala a
Mpingo wa Mulungu amakhulupirira Khristu
Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, Apulumutsi
mu m’badwo wa Mzimu Woyera, ndipo adamvera mawu Awo.
Zotsatira zake, ntchito yodabwitsa ya uthenga
wabwino ikuchitika padziko lonse lapansi.
Ndikweza maso anga kumapiri:
Thandizo langa lidzera kuti?
Thandizo langa lidzera kwa Yehova,
wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Masalimo 121:1-2
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi