Ngakhale lero, mu lamulo la Mulungu
losunga pangano latsopano monga tsiku
la Sabata ndi Paska, pali chifuniro Chake chakuya
chofanana ndi pamene Mulungu anauza Adamu
ndi Heva m’munda wa Edeni kuti, “Musadye
zipatso za mtengo wakudziwitsa
chabwino ndi choipa” kuti awadalitse.
Lili ndi chifuniro chachikulu
chakupereka madalitso kwa anthu
kupyolera m’pangano latsopano.
Ngati tingodalira zomwe takumana nazo
komanso chidziwitso chathu ndikuwona
mawu a Mulungu kukhala otsika, zovuta ndi
matsoka zidzatitsatira pamapeto pake.
Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi
atiphunzitsa kuti pamene tiwona mawu a Mulungu
kukhala amtengo wapatali monga momwe Daniele,
Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anachitira,
tidzalandira madalitso ndi ulemerero
umene udzadabwitsa dziko lapansi.
Muzisamalira kuchita malamulo onse
amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale
ndi moyo, ndi kuchuluka, ndi kulowa, ndi
kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.
Deuteronomo 8:1
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a
Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi
kusamalira kuchita malamulo ake onse
amene ndikuuzani lero, kuti Yehova
Mulungu wanu adzakukulitsani koposa
amitundu onse a padziko lapansi;
Deuteronomo 28:1
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi