M’busa ndi wofunika kwambiri kuposa
mfumu kwa nkhosa yotayika, ndipo
madzi ndi ofunika kwambiri
kuposa golide mu m’chipululu.
Ubwino wa malamulo a Mulungu
udzaonekera pamene anthu adzaimirira
pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Mulungu.
Izi zili choncho chifukwa kumwamba ndi ku
gehena zimatsimikiziridwa potengera ngati
munthu wasunga malamulo a Mulungu kapena ayi.
Popeza kuti Ufumu wa Kumwamba ndi
malo amene ochimwa sangalowemo,
m’pofunika kuti alandire
chikhululukiro cha machimo awo.
Mulungu walonjeza kukhululukidwa kwa
machimo m’mwazi wamtengo wapatali wa
Kristu kudzera m’pangano latsopano la Paska.
Chotero, mofanana ndi Davide,
anthu ayenera kukhulupirira lonjezo la
Mulungu ndi kukonda malamulo Ake.
Chifukwa chake ndikonda malamulo anu
koposa golide, inde golide woyengeka. . . .
Masalimo 119:127
[M]ukati kwa Iye, Mphunzitsi anena,
Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya
Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
Ndipo ophunzira anachita monga
Yesu anawauza, nakonza Paska.
. . . Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi
ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa
chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.
Mateyu 26:18-28
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi