M’moyo wathu wonse, tonse timakumana ndi mavuto osiyanasiyana.
Munthawi zamavuto oterowo, makolo akale achikhulupiriro
m’badwo wa Atate anaitana pa Yehova Mulungu ndipo
anapulumutsidwa, oyera mtima mu m’badwo wa Mwana
anaitana pa dzina la Yesu Khristu ndipo anapulumutsidwa,
ndipo mu m’badwo wa Mzimu Woyerayo, tiyenera kuitana
pa Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi kuti tipulumutsidwe.
Mulungu ananena kuti amene akudziwa dzina lake ndi anthu Ake enieni, ndipo
anatilamulira kuchita ubatizo, womwe ndi sitepe yoyamba ya chipulumutso,
m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.
Masiku ano, Gulu la Utimiki wa Dziko Lonse Mpingo wa Mulungu wokha ndiwo
umabatiza anthu mdzina la Mzimu Woyera Khristu Ahnsahnghong, lomwe lili ndi lonjezo
la chipulumutso ndi chikhululukiro cha machimo.
Pakuti Ambuye Yehova atero, . . . Chifukwa chake anthu anga adzadziwa
dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene
ndinena; taonani, ndine pano.
Yesaya 52:4–6
Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, . . .
ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa
Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, . . .
Chivumbulutso 3:12
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi