Monga Yesu Khristu anatsika Kumwamba kubwera pa dziko lapansi ndi kukwera Kumwamba, anthu amene amakhulupirira Mulungu pa dziko lapansi ayeneranso kubwerera Kumwamba. Chofunikira kuti munthu akalowe mu Ufumu wa Kumwamba ndi kulandira moyo wosatha.
Anthu angathe kupita Kumwamba kumene kulibe imfa pokhapokha atalandira moyo wosatha umene Mulungu analonjeza. Moyo wosatha ndi wololedwa kwa okhawo amene amadya thupi la Yesu ndi kumwa mwazi Wake kudzera pa Paska wa Pangano Latsopano.
Ngakhale chikhulupiriro chathu chingakhale chachikulu chotani, sitingalandire moyo wosatha pokhapokha titasunga Paska.
Mpingo wa Mulungu ndi mpingo wokhawo pa dziko lapansi umene umasunga Pangano Latsopano.
Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu. Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
Ahebri 10:35–36
Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.
1 Yohane 2:25
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi